Company Logo

SIA Tech-Print Media

Home Islamic Resources and Programs High Quality Document Services Computer Repair Specialist Phone Repair Specialist Selling Products Computer & Phone Software Problems? Computer Classes Contact
Machilitso a chisilamu | SIA Tech-Print Media
Machilitso a chisilamu
Image

Description:

MAU OYAMBA
?????? ??????? ??????????? ??????????
Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah yemwe anatsitsa Buku la Qur’aan kukhala machilitso komanso chifundo kwa Okhulupilira,
Ndikuchitira umboni kuti palibe Mulungu wina oyenera kupembezedwa mwa choonadi koma Allah yekha amene amachiza odwala ndikupereka chilimbikitso kwa ofooka komansp kuwongolera munthu kunjira ya chiwongoko.
Ndikuchitiranso umboni kuti Muhammad (SAW)Ndi kapolo Wa Allah komanso Mtumiki Wake.
Madalitso ndimtendere za Allah zipite kwa Mtumiki Wathu Muhammad(SAW)Amene adatilongosolera kalikonse kachipembezo ndipo sadasiye kanthu.Madalitso amenewa apitenso kwa akubanja ake komanso Ophunzira ake osaiwalanso asilamu tonse omwe tikutsata njira yamtumiki mwaubwino mpaka tsiku la chiweluzo.
Pambuyo pa mau amenewa.
Uku ndikulemba koyamba kwa buku limeneri la Machilitso Ovomerezeka A Chisilamu ndipo ndalikonza komanso kulitanthawuzira ndicholinga choti anthu ena omwe sadziwa chiyankhulo cha chiarabu bwino bwino athe kupindura nawo.
Ntchito yolemba bukuli sidali yophweka kuti itheke ayi koma kuti Allah ndi amene wazichita kukhala zophweka kutero.Ndidali osamalisitsa zedi kuti pasapezeke chinthu chofooka mubukuli ndichifukwa ndatenga ma dua ovomelezeka pamachilitso ndikuziyika kuti zikhale zopindura kwa Anthu.
Bukuli Ndayikamo mitundu iwiri ya machilitso mmene zimayenera kukhalira ndipo machilitso oyamba ndi ochokela ku Qur’aan yolemekezeka pamene machilitso achiwiri ndi ochokera mu Sunnah Ya Mtumiki (SAW) Ndipo Gawo lamachilitso a Sunnah ndalembamo ma dua otsimikizika umboni wake ndicholinga chowapatsa owerenga chidwi ndikutsimikizika pa bukuli.Ndizofunika kwambiri kuchitira chidwi kuliwelenga bukuli chifukwa Kutengera munyengo zino kwachuluka anthu omwe akutsogolera ku njira yoipa pobisalira kumachilitso osadziwa kuti ali mu mpingo wa Satana,Pempho langa kwa aliyense oliwerenga ndiloti tsatani chilichonse chomwe mwalangizidwa kuti machilitso akhale ovomelezeka kukuli ndikhala ndikuonjezeramo maphindu ena osiyana siyana ndipo ndili okonzeka kukonza zolakwika zomwe zingapezeke mubukuli kumbari za kalembedwe,Ndikupempha Allah kuti apeleke malipiro antchito imeneyi kwa Mayi anga komanso Bambo anga amene adagwira ntchito yaikulu kulimbana nane pondiphunzitsa ndipo sanatope kundilangiza za kulimbikira Maphunziro a chipembezo chachisilamu,Komanso malipiro amenewo apite kwaine komanso banja langa,abale anga ndi asilamu onse,ndikupemphanso Allah kuti ayipange ntchito imeneyi kukhala yovomelezeka kwa Iye Aamiin.
Allah nde mwini uzindikiri ndipo kwaiye ndikomwe ndayezamira
Ustaadh Shuaibu Idi Affaan.

Uploaded on: 2025-04-23

Category: Islamic Resources and Programs

View PDF Download PDF